Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Dziteteni kwa Anthu Ampatuko

Dziteteni kwa Anthu Ampatuko

Satana komanso anthu amene ali kumbali yake, nthawi zambili amafalitsa mabodza pofuna kufooketsa cikhulupililo cathu. (2 Mbiri 11:3) Mwacitsanzo, Asuri anagwilitsa nchito mfundo zosoceletsa, komanso mabodza amkunkhuniza pofuna kufooketsa anthu a Yehova (2 Mbiri 32:10-15) Izi n’zimenenso ampatuko amacita masiku ano. Kodi tiyenela kuziona bwanji ziphunzitso za ampatuko? Tiyenela kuziona kuti ni zovulaza mofanana na poizoni! Sitiyenela kuziŵelenga ziphunzitso zimenezo kapena kunenapo ciliconse. Komanso sitiyenela kuzitumiza kwa ena kapena kuwafotokozelako. Cinanso, muziyesetsa kuzindikila mwamsanga mfundo zabodza zimene zingakupangitseni kukayikila Yehova na gulu lake, ndipo zikaneni!—Yuda 3, 4.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI “MENYANI MWAMPHAMVU NKHONDO YA CIKHULUPILILO”!—MBALI YAKE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’cifukwa ciyani tiyenela kukhala osamala pogwilitsa nchito mawebusaiti a makambilano?

  • Kodi tingatsatile bwanji ulangizi wa pa Aroma 16:17?