Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pezani Cimwemwe Poyambitsa Makambilano

Pezani Cimwemwe Poyambitsa Makambilano

Kuceza na anthu kuti tiwalalikile mwamwayi ni imodzi mwa njila zosangalatsa kwambili komanso zogwila mtima zocitila umboni. Ngakhale n’telo, tingacite mantha kuyambitsa makambilano ngati tiganizila kwambili za mmene tingaloŵetselepo mfundo ya m’Baibo. M’malo modela nkhawa kuti mukamba naye ciyani munthu pomulalikila, ganizilani kwambili mmene mungamuonetsele cidwi. (Mat. 22:39; Afil. 2:4) Ngati pamene mukambilana, mpata wapezeka wakuti mumuuzeko za cikhulupililo canu, pali zida zambili zimene zingakuthandizeni.

Kodi zida zotsatilazi zingakuthandizeni bwanji kuti mulalikile pankhani imene yayambika poceza na munthu?

TAMBANI VIDIYO YAKUTI CITSULO CIMANOLA CITSULO CINZAKE” —KUYAMBITSA MAKAMBILANO, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

Ni mfundo zitatu ziti zimene zingatithandize kukulitsa luso lokambilana na anthu?