Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRITU

Muzidziona Mmene Yehova Amakuonelani

Muzidziona Mmene Yehova Amakuonelani

“Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, Yehova amaona makhalidwe athu abwino komanso zimene tingakwanitse kucita. Komabe, nthawi zina zingativute kudziona mmene Yehova amationela. Tikhoza kumadziona ngati osafunika cifukwa ca mmene anthu ena amacitila nafe zinthu. Mwinanso cifukwa coganizila kwambili zolakwa zathu zakale, tingayambe kukayikila zakuti Yehova amatikondadi. N’ciyani cingatithandize tikayamba kudziona motelo?

Tizikumbukila kuti Yehova amatha kuona zimene ife anthu sitingathe kuona. (1 Sam. 16:7) Izi zitanthauza kuti iye amaona zambili mwa ife kuposa zimene ife eni tingaone. Cokondweletsa n’cakuti Baibo imatithandiza kudziŵa mmene Yehova amationela. Tingadziŵe zimenezi mwa kuŵelenga malemba na nkhani za m’Baibo, zoonetsa kuti Yehova amawakonda kwambili alambili ake.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI TSIMIKIZILANI MTIMA WANU KUTI YEHOVA AMAKUKONDANI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi citsanzo ca tate na mwana wake wothamanga citiphunzitsa ciyani za mmene Yehova amationela?

  • Ngati munthu anacita chimo lalikulu koma anacitapo kanthu kuti akonzenso ubwenzi wake na Yehova, kodi angautsimikizile bwanji mtima wake kuti Mulungu sakumuimba mlandu?—1 Yoh. 3:19, 20

  • Kodi m’bale wa mu vidiyoyi anapindula bwanji ataŵelenga na kusinkhasinkha nkhani za m’Baibo za Davide na Yehosafati?