Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova ni “Tate wa Ana Amasiye”

Yehova ni “Tate wa Ana Amasiye”

Caka ciliconse, acicepele ambili amasankha kukhala mabwenzi a Yehova. (Sal. 110:3) Yehova amasamala kwambili za aliyense wa inu acicepele. Amamvetsa mavuto amene mukukumana nawo, ndipo walonjeza kuti adzakuthandizani kumutumikila. Ngati muli m’banja la kholo limodzi, kumbukilani kuti Yehova ni “Tate wa ana amasiye.” (Sal. 68:5) Yehova adzakuphunzitsani, moti mudzakwanitsa kumutumikila mosasamala kanthu mmene zinthu zilili pa nyumba panu.—1 Pet. 5:10.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI OMENYA NKHONDO YACIKHULUPILILO MWACIPAMBANO—AMENE AKULELEDWA NA KHOLO LIMODZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi tiphunzilapo ciyani pa zitsanzo za Tammy, Charles, na Jimmy?

  • Kodi pa Salimo 27:10 pali mfundo yotani yolimbikitsa kwa ana amene akuleledwa na kholo limodzi?