CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khulupililani Yehova Mulungu Wanu”
Atawopsezedwa, Yehosafati na anthu a ku Yuda anapemphela kwa Yehova kuti awathandize (2 Mbiri 20:12, 13; w14 12/15 23 ¶8)
Yehova analimbikitsa anthu ake na kuwapatsa malangizo omveka bwino (2 Mbiri 20:17)
Yehova anapulumutsa anthu ake cifukwa anamukhulupilila (2 Mbiri 20:21, 22, 27; w21.11 16 ¶7)
Pamene Gogi adzaukila anthu a Yehova pa cisautso cacikulu, awo amene adzapitiliza kukhulupilila Yehova na kudalila anthu amene iye akuwagwilitsa nchito potsogolela, sadzaopa ciliconse.—2 Mbiri 20:20.