Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kodi Mwakonzeka Kukumana na Mavuto a Zacuma?

Kodi Mwakonzeka Kukumana na Mavuto a Zacuma?

Nthawi zina zocitika za padzikoli zimayambitsa mavuto a zacuma padziko lonse. Sitidabwa na zimenezi cifukwa tikukhala cakumapeto kwenikweni kwa masiku otsiliza, ndipo Baibo imaticenjeza kuti sitiyenela kudalila “cuma cosadalilika.” (1 Tim. 6:17; 2 Tim. 3:1) Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Mfumu Yehosafati pa nkhani yokonzekela mavuto a zacuma?

Atawopsezedwa na adani, Yehosafati anadalila Yehova. (2 Mbiri 20:9-12) Komanso anakonzekeletsa mtundu wa Yuda mwa kumanga mipanda yolimba kwambili na misasa ya asilikali. (2 Mbiri 17:1, 2, 12, 13) Mofanana na Yehosafati, tiyenela kudalila Yehova na kukonzekela pasadakhale tisanakumane na mavuto.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKELA TSOKA LA ZACILENGEDWE? KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’ciyani cimene aliyense wa ife angacite pokonzekela tsoka?

     
  • Kodi tingakonzekele bwanji kuthandiza ena pakagwa tsoka?