May 13-19
MASALIMO 38-39
Nyimbo 125 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Musamadziimbe Mlandu Mopitilila Malile
(Mph. 10)
Kudziimba mlandu mopitilila malile kuli ngati kunyamula cikatundu colemetsa (Sal. 38:3-8; w20.11 27 ¶12-13)
M’malo mongoganizila zolakwa zanu zakale, muziyesetsa kucita zinthu zokondweletsa Yehova (Sal. 39:4, 5; w02-CN 11/15 20 ¶1-2)
Muzipemphela ngakhale kuti nthawi zina cingakhale covuta cifukwa codziimba mlandu (Sal. 39:12; w21.10 15 ¶4)
Ngati mumadziimba mlandu mopitilila malile, kumbukilani kuti Yehova “adzamukhululukila ndi mtima wonse” munthu wocimwa akalapa.—Yes. 55:7.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 39:1—Ni pa nthawi iti pamene tingagwilitse nchito mfundo yakuti ‘tidzaphimba pakamwa pathu’? (w22.09 13 ¶16)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 38:1-22 (th phunzilo 2)
4. Kukhala Wosamala—Mmene Paulo Anacitila Zimenezi
(Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO, kenako kambilanani lmd phunzilo 5 mfundo 1-2.
5. Kukhala Wosamala—Tengelani Citsanzo ca Paulo
(Mph. 8) Makambilano ozikika mu lmd phunzilo 5 mfundo 3-5, komanso mbali yakuti “Onaninso Malemba Awa.”
Nyimbo 44
6. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 15)
7. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 9 ¶17-24, bokosi pa tsa. 73