Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

“Mwamuna Wake Amadziŵika Pazipata”

“Mwamuna Wake Amadziŵika Pazipata”

Mkazi wabwino amapeleka cithunzi cabwino ca mwamuna wake. M’masiku a Mfumu Lemueli, mwamuna amene anali na mkazi wabwino anali ‘kudziŵika pazipata.’ (Miy. 31:23) Masiku ano, amuna a mbili yabwino amatumikila monga akulu ndi atumiki othandiza. Ngati ni okwatila, utumiki wawo umadalila kwambili pa khalidwe labwino la akazi awo ndi thandizo lawo. (1 Tim. 3:4, 11) Akazi a conco amayamikilidwa kwambili ndi amuna awo ndiponso mpingo.

Mkazi wabwino amathandiza mwamuna wake kutumikila mwa. . .

  • kumulimbikitsa na mau abwino.—Miy. 31:26

  • kugaŵana mwamuna wakeyo ndi mpingo.—1 Ates. 2:7, 8

  • kukhala na umoyo wosalila zambili.—1 Tim. 6:8

  • kusamufunsa zinsinsi za mumpingo.—1 Tim. 2:11, 12; 1 Pet. 4:15