UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Mmene Tingaseŵenzetsele Buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse n’lolingana ni buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa. Mabuku onse aŵiliwa ni zida zophunzitsila zimene zimafotokoza mfundo zofanana za coonadi m’njilanso yofanana. Komabe, buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse lili na mau osavuta kumva ndipo limafotokoza zinthu m’njila yosavuta kumva. Linapangidwila anthu amene zimawavuta kumvetsetsa buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa. Buku limeneli lili na Zakumapeto zimene zipeleka matanthauzo osavuta a mau ena opezeka m’bukuli. Nkhani iliyonse ilibe mafunso kuciyambi kapena bokosi lobwelelamo kumapeto. M’malomwake, kumapeto kwa nkhani iliyonse kuli mfundo zikulu za coonadi ca m’Baibo zimene zakambidwa m’nkhaniyo. Mofanana ndi buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa, buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse lingagaŵilidwe nthawi iliyonse ngakhale kuti silili pa m’ndandanda wa zogaŵila za mweziwo. Tingaseŵenzetse bwanji zinthu zatsopano za m’bukuli pocititsa phunzilo la Baibo?
MFUNDO ZIKULU: Nthawi zambili tikamaphunzila na anthu m’buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa, timaŵelenga ndime ndi kufunsa mafunso. Njila imeneyi ingakhalenso yothandiza kwa anthu ambili pamene tiphunzila nawo buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. Nanga bwanji ngati wophunzila sadziŵa bwino cinenelo kapena amavutika kuŵelenga? Ngati n’conco, mukhoza kumaseŵenzetsa buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse. Ndiyeno cigawo cakuti Mfundo Zikulu, mungaciseŵenzetse monga maziko a phunzilo lanu ndipo mungalimbikitse wophunzila kuti aziŵelenga nkhani yonse payekha. Kuphunzitsa munthu mfundo iliyonse ya coonadi ca m’Baibo ya pa cigawo cimeneci, kungatenge pafupi-fupi mphindi 15. Popeza kuti cigawo ca mfundo zikulu sicikhala na mfundo zonse za m’nkhani, mufunika kukonzekela bwino ndi kuganizila zosowa za wophunzila wanu. Ngati pocititsa phunzilo museŵenzetsa nkhani yonse, mungakambilane cigawo ca mfundo zikulu pobweleza zimene mwaphunzila.
ZAKUMAPETO: Mau a zakumapeto alembedwa motsatila ndondomeko ya nkhani za m’bukuli. Pocititsa phunzilo, mphunzitsi angasankhe kukambilana ndi wophunzila wake zakumapeto m’buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse.