UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Acicepele—Musazengeleze Kuloŵa pa ‘Khomo Lalikulu’
N’capafupi kuona ngati tidzakhalabe acicepele ndipo “masiku oipa” amene amabwela cifukwa ca ukalamba m’dziko la Satanali, sangatifikile. (Mlal. 12:1) Ngati ndinu wacicepele, kodi mukuzengeleza kuyambako mautumiki monga utumiki wa nthawi zonse poganiza kuti mukali na nthawi yambili?
Tonse ‘zinthu zosayembekezeleka zimatigwela.’ (Mlal. 9:11) “Simukudziŵa kuti moyo wanu udzakhala wotani mawa.” (Yak. 4:14) Conco, musazengeleze kuyambako mautumiki osiyana-siyana malinga ndi zolinga zanu zauzimu. Loŵani pa “khomo lalikulu la mwayi wautumiki” likali lotseguka. (1 Akor. 16:9) Mukacita zimenezo, simudzadandaula.
Zolinga zauzimu zimene mungakhale nazo:
-
Kulalikila anthu okamba cinenelo cina
-
Upainiya
-
Kuloŵa masukulu ophunzitsa atumiki a Mulungu
-
Nchito ya zomanga-manga
-
Kutumikila pa Bateli
-
Kuyang’anila dela