Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Maulaliki a Citsanzo

Maulaliki a Citsanzo

NSANJA YA MLONDA

Funso: Munthu atakufunsani kuti kumwamba kuli ciani, mungayankhe bwanji?

Lemba: Yoh. 8:23

Cogaŵila: Nsanja ya Mlonda iyi ikamba zimene Yesu na Atate ŵake atiuza ponena za kumwamba.

PHUNZITSANI COONADI

Funso: Kodi mau a ulosi awa opezeka m’Baibo agwilizana na zimene zicitika masiku ano?

Lemba: 2 Tim. 3:1-5

Mfundo ya Coonadi: Popeza kuti ulosi wa m’Baibo wokamba za masiku otsiliza ukukwanilitsidwa masiku ano, sitingakayikile kuti nawonso ulosi wokamba za tsogolo labwino udzakwanilitsidwa.

N’CIFUKWA CIANI MUYENELA KUPHUNZILA BAIBULO? (Vidiyo)

Mau oyamba: Titambitsa anthu kavidiyo kamene kakamba za kumene tingapeze mayankho a mafunso ofunika kwambili paumoyo. (Tambitsani mwininyumba kavidiyo kameneka.)

Cogaŵila: Buku ili lifotokoza mmene Mulungu adzathetsela mavuto padziko lapansi malinga n’zimene Baibo imakamba. (Gaŵilani buku la Zimene Baibo Imaphunzitsa kapena Zimene Baibulo Ingatiphunzitse.)

KONZANI ULALIKI WANU

Funso:

Lemba:

Cogaŵila: