Anthu obwela ku msonkhano wacigawo ku Malawi, asonkhana pamodzi m’madzulo, ndipo akutamba pulogilamu ya JW Broadcasting

UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO November 2019

Makambilano Acitsanzo

Makambilano otsatizana-tsatizana okamba za colinga ca Mulungu na malonjezo ake a kutsogolo.

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Musamakonde Dziko Kapena Zinthu za M’dziko

N’ciani cingatithandize kupewa kutengeka na dziko na zokopa zake kuti tisacoke kwa Yehova?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati

Ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingathandize oloŵa m’banjawo kukonzekela tsiku lapadela limeneli, m’njila yakuti asadzakhale na cikumbumtima covutitsidwa kapena kudziimba mlandu pambuyo pake?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Tifunika Kumenya Nkhondo kuti Tikhalebe m’Coonadi

Kodi tingamenye bwanji “mwamphamvu nkhondo yacikhulupililo”?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Ndikudziŵa Nchito Zako”

Yesu adziŵa zonse zimene zikucitika m’mipingo ndipo amadziŵa ciliconse cokhudza akulu mu mpingo.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Adziŵa zimene Tifunikila

N’cifukwa ciani msonkhano wacigawo umakhala cakudya ca panthawi yake? N’ciani cimapangitsa misonkhano ya mkati mwa wiki kukhala yolimbikitsa komanso yothandiza?

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Amuna Anayi Okwela pa Mahosi

Masiku ano tikucitila umboni za amuna anayi ophiphilitsila okwela pa mahosi ochulidwa m’buku la Chivumbulutso. Kodi wokwela pa hosi aliyense akuimila ciani?

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Amakonda Munthu Wopeleka Mokondwela

Kodi tingacite bwanji zopeleka kuti ticilikize nchito ya Mboni za Yehova, m’dziko lathu komanso padziko lonse?