Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 YOHANE 1-13; 3 YOHANE 1-14-YUDA 1-25

Tifunika Kumenya Nkhondo kuti Tikhalebe m’Coonadi

Tifunika Kumenya Nkhondo kuti Tikhalebe m’Coonadi

Yuda 3

Yesu anatiilimbikitsa kuti: “Yesetsani mwamphamvu kuloŵa pakhomo lopapatiza.” (Luka 13:24) Mawu a Yesu aonetsa kuti tifunika kulimbikila, kuyesetsa kuti Mulungu atiyanje. Yuda m’bale wake wa Yesu, anauzilidwa kulemba mawu ofanana na amenewa. Anati: ‘Menyani mwamphamvu nkhondo yacikhulupililo.’ Timafunika kuyesetsa mwakhama kuti tikwanitse kucita zotsatilazi:

  • Kupewa dama.—Yuda 6, 7

  • Kulemekeza amene ali na ulamulilo.—Yuda 8, 9

  • Kudalila kwambili ziphunzitso zozikidwa pa “cikhulupililo . . . coyela kopambana,” kutanthauza ziphunzitso zacikhristu.—Yuda 20, 21