Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 1–3

“Ndikudziŵa Nchito Zako”

“Ndikudziŵa Nchito Zako”

1:20; 2:1, 2

  • “Nyenyezi 7”: Akulu odzozedwa komanso akulu onse

  • “M’dzanja [la Yesu] lamanja”: Yesu ndiye ali na mphamvu, ulamulilo na citsogozo pa nyenyezi zimenezo. Ngati wina m’bungwe la akulu afunika kuwongoleledwa, Yesu amaonetsetsa kuti zimenezi zacitika pa nthawi yake komanso m’njila yoyenela

  • “Zoikapo Nyale 7 Zagolide”: Mipingo yacikhristu. Monga mmene coikapo nyale ca m’cihema cinali kuunikila, mipingo yacikhritsu imaunikila coonadi cocokela kwa Mulungu. (Mat. 5:14) Yesu ni “woyenda pakati” pa zoikapo nyale m’njila yakuti, ndiye amayang’anila zocitika za m’mipingo yonse