Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Adziŵa zimene Tifunikila

Yehova Adziŵa zimene Tifunikila

Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amatipatsa cakudya “pa nthawi yoyenela,” kuonetsa kuti Yehova, amene akutsogolela kapoloyo, adziŵa zimene timafunikila mwauzimu. (Mat. 24:45) Cakudya ca pa nthawi yoyenela ciphatikizapo misonkhano yacigawo na misonkhano ya mkati mwa wiki.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI YA 2017 YA KOMITI YOYANG’ANILA NCHITO YOPHUNZITSA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • N’ndani amene ayenela kulandila citamando kaamba ka misonkhano yacigawo ya pa nthawi yake imene timakhala nayo? Cifukwa ciani?

  • Kodi nchito yokonzekela msonkhano wacigawo imayamba liti?

  • Kodi amasankha bwanji mitu na nkhani za misonkhano yacigawo?

  • Kodi pamakhala nchito zotani pokonzekela misonkhano yacigawo?

  • Kodi njila zophunzilila za m’sukulu ya Giliyadi amaziseŵenzetsa bwanji pokonza nkhani zophunzila pa misonkhano ya mkati mwa wiki?

  • Kodi madipatimenti osiyana-siyana amaseŵenzela bwanji pamodzi pokonza kabuku ka misonkhano?

Kodi mumamvela bwanji cifukwa ca zinthu zauzimu zimene Yehova amatipatsa?