Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

November 25–December 1

CHIVUMBULUTSO 4-6

November 25–December 1
  • Nyimbo 22 na Pemphelo

  • Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Amuna Anayi Okwela pa Mahosi”: (10 min.)

    • Chiv. 6:2—Wokwela pa hosi yoyela ‘anapita kukagonjetsa adani ake’ (wp17.3 4 ¶3, 5)

    • Chiv. 6:4-6—Ndiyeno panabwela wokwela pa hosi yofiila, ndiponso wokwela pa hosi yakuda (wp17.3 5 ¶2, 4-5)

    • Chiv. 6:8—Pambuyo pake, panabwela wokwela pa hosi yotuŵa, ndipo Manda anali kumutsatila (wp17.3 5 ¶8-10)

  • Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)

    • Chiv. 4:4, 6—Kodi akulu 24 na zamoyo zinayi amaimila ciani? (re 76-77 ¶8; 80 ¶19)

    • Chiv. 5:5—N’cifukwa ciani Yesu amachulidwa kuti “Mkango wa fuko la Yuda”? (cf 36 ¶5-6)

    • Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?

    • Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?

  • Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Chiv. 4:1-11 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

  • Nyimbo 46

  • Yehova Amakonda Munthu Wopeleka Mokondwela”: (15 min.) Nkhani yokambiwa na mkulu. Yambani mwa kutambitsa vidiyo yakuti Mmene Mungapelekele Zopeleka pa Intaneti. Fotokozelani ofalitsa kuti angadziŵe zambili zokhudza kucita copeleka mwa kutinika pambali yakuti Zopeleka pa jw.org na pa JW Library kapena kulemba kuti Copeleka.pr418.com pa malo oikapo adresi. Ndiyeno ŵelengani kalata yaciyamikilo yocokela ku Ofesi ya Nthambi yoyamikila zopeleka zimene abale anacita caka catha ca utumiki. Yamikilani mpingo cifukwa ca mtima wawo wocilikiza moolowa manja.

  • Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 92

  • Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)

  • Nyimbo 43 na Pemphelo