Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 4-6

Amuna Anayi Okwela pa Mahosi

Amuna Anayi Okwela pa Mahosi

6:2, 4-6, 8

Yesu ‘anapita kukagonjetsa adani ake’ mwa kumenya nkhondo na Satana ndi ziŵanda zake kumwamba na kuziponya pa dziko lapansi. Yesu akupitiliza kugonjetsa adani ake mwa kuthandiza na kuteteza atumiki ake m’masiku otsiliza ano. Pa Aramagedo, iye ‘adzapambana pa nkhondo yolimbana nawo’ pamene adzacotsapo amuna atatu okwela pa mahosi, komanso pamene adzakonza zinthu zimene iwo awononga.