Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Amakonda Munthu Wopeleka Mokondwela

Yehova Amakonda Munthu Wopeleka Mokondwela

Pa 2 Akorinto 9:7, pamati: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” Masiku ano, pali njila zosavuta zocitila copeleka pa intaneti kuti ticilikize nchito ya Mboni za Yehova, m’dziko lathu komanso padziko lonse.

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MMENE MUNGAPELEKELE ZOPELEKA PA INTANETI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AYA:

  • Kodi peji yofotokoza njila za mocitila copeleka m’dziko lathu tingaipeze bwanji?

  • Kodi ena apindula bwanji cifukwa cocita copeleka kupitila pa intaneti?

  • Ni njila zina ziti zimene tingaseŵenzetse pocita copeleka?

  • Tingacite ciani ngati sitidziŵa kuseŵenzetsa njila za pa intaneti zimenezi?