Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati

Pewani Kutengela Maganizo a Dziko Pokonzekela Cikwati

M’bale na mlongo amene ali pa citomelo, amafunika kupanga zosankha zambili pokonzekela cikwati cawo. Iwo angafunitsitse kucita cikwati capamwamba monga mmene vikwati vina vimacitikila m’dela lawo. Mabwenzi komanso acibululu, angakhale na maganizo awo pa zinthu zimene ziyenela kuloŵetsedwamo pokonzekela cikwati. Kodi ni mfundo ziti za m’Baibo zimene zingathandize oloŵa m’banjawo kukonzekela tsiku lapadela limeneli, m’njila yakuti asadzakhale na cikumbumtima covutitsidwa kapena kudziimba mlandu pambuyo pake?

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MAUKWATI AMENE AMALEMEKEZA YEHOVA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSTILAWA:

  • Kodi mfundo za m’Baibo pa Malemba otsatilawa zinathandiza bwanji Nick na Juliana?

    • 1 Akor. 10:31

    • 1 Yoh. 2:15, 16

    • Agal. 5:19-21

    • 1 Tim. 2:9

  • N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi amene afuna kucita cikwati ayenela kusankha m’bale wokhwima mwauzimu kuti akhale “woyang’anila phwando”?—Yoh. 2:9, 10.

  • N’cifukwa ciani Nick na Juliana anasankha kuti cikwati cawo cicitike mwanjila imeneyo?

  • N’ndani ali na udindo wopanga zosankha zokhudza phwando la cikwati komanso kocitila?—w06 10/15 25 ¶10