Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

November 16-22

LEVITIKO 4-5

November 16-22
  •  Nyimbo 84 na Pemphelo

  •  Mawu Oyamba (1 min.)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • M’patseni Zabwino Koposa Yehova”: (10 min.)

    • Lev. 5:5, 6—Anthu amene acita macimo enaake anali kufunika kupeleka mwana wa nkhosa kapena mbuzi monga nsembe yopalamula (it-2 527 ¶9)

    • Lev. 5:7—Amene sanakwanitse kupeleka mwana wa nkhosa kapena mbuzi cifukwa cosauka, anali kupeleka njiwa ziŵili kapena nkhunda ziŵili (w09 6/1 26 ¶3)

    • Lev. 5:11—Amene analephela kupeleka ngakhale njiwa ziŵili kapena nkhunda ziŵili cifukwa cosauka, anali kupeleka ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa (w09 6/1 26 ¶4)

  • Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)

    • Lev. 5:1—Kodi vesi imeneyi igwila nchito bwanji kwa Akhristu? (w16.02 24¶14)

    • Lev. 5:15, 16—Kodi zinali kucitika bwanji nthawi zina kuti munthu acite “mosakhulupilika mwa kucimwila zinthu zopatulika za Yehova mosadziŵa”? (it-1 1130 ¶2)

    • Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?

  • Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Lev. 4:27–5:4 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

  • Nyimbo 81

  • Tacita Upainiya Pamodzi kwa Zaka 60 na Thandizo la Yehova: (15 min.) Tambitsani vidiyo imeneyi. Pambuyo pake, funsani mafunso aya: Kodi ni mwayi wotani komanso zinthu zokondweletsa ziti zimene mlongo Takako na mlongo Hisako anasangalala nazo mu utumiki wawo? Ni mavuto ati okhudza thanzi amene mlongo Takako ali nawo, nanga cam’thandiza n’ciani? N’ciani cawathandiza kupeza cimwemwe ceni-ceni na kukhala okhutila? Kodi mbili ya umoyo wawo itsimikizila bwanji mfundo za pa malemba aya: Miyambo 25:11; Mlaliki 12:1; Aheberi 6:10?

  • Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) lfb phunzilo 1, 2

  • Mawu Othela (3 min olo kucepelapo)

  • Nyimbo 11 na Pemphelo