EKSODO 39-40
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU |Mose Anatsatila Malangizo Mosamala
39:32, 43; 40:1, 2, 16
Mose anatsatila mosamala malangizo a tsatane-tsatane amene Yehova anam’patsa a mmene anafunika kumangila cihema na kuciutsa. Nafenso tiyenela kumvela malangizo alionse amene timalandila m’gulu la Yehova, na kuwatsatila mwamsanga komanso na mtima wonse. Kucita zimenezi n’kofunika olo malangizo aoneke monga osafunika kapena ngati sitimvetsetsa cifukwa cimene atipatsila malangizowo.—Luka 16:10.
N’cifukwa ciani tiyenela kumvetsela na kutsatila mosamala malangizo amene timalandila . . .
-
pa kukumana kokonzekela ulaliki?
-
okhudza kukonzekela matenda a mwadzidzidzi?
-
okhudza kukonzekela matsoka a zacilengedwe?