November 30–December 6
LEVITIKO 8-9
Nyimbo 16 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Umboni wa Dalitso la Yehova”: (10 min.)
Lev. 8:6-9, 12—Mose analonga ansembe (it-1 1207)
Lev. 9:1-5—Mtundu wa Aisiraeli unalipo pamene ansembewo anapeleka nsembe zanyama kwa nthawi yoyamba (it-1 1208 ¶8)
Lev. 9:23, 24—Yehova anaonetsa kuti anawavomeleza ansembewo (w19.11 23 ¶13)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Lev. 8:6—Mulungu anali kufuna kuti ansembe azikhala oyela. Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? (w14 11/15 9 ¶6)
Lev. 8:14-17—Pa nthawi yolonga ansembe, n’cifukwa ciani Mose ndiye anapeleka nsembe osati Aroni? (it-2 437 ¶3)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Lev. 8:31–9:7 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno muonetseni mwininyumba mfundo inayake ya m’magazini yogaŵila ya Nsanja ya Mlonda ya Na. 2 2020, na kum’gaŵila magaziniyo. (th phunzilo 6)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno m’fotokozeleni za webusaiti yathu mwininyumba, na kumusiila kakhadi kongenela pa jw.org. (th phunzilo 4)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 84 ¶6-7 (th phunzilo 11)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kulalikila Pafoni”: (15 min.) Nkhani yokambilana yokambidwa na woyang’anila utumiki. Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) lfb phunzilo 5, 6
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 150 na Pemphelo