Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 8–9

Umboni wa Dalitso la Yehova

Umboni wa Dalitso la Yehova

8:6-9, 12; 9:1-5, 23, 24

Yehova anagwetsa moto umene unanyeketsa nsembe zopseleza zimene ansembe a m’banja la Aroni anapeleka atangolongedwa unsembe. Izi zinaonetsa kuti Yehova anawavomeleza ansembewo komanso kuti anali kuwacilikiza. Mwa kucita zimenezi, Yehova analimbikitsa Aisiraeli amene anasonkhana na kuona zocitikazo kuti aziwacilikiza na mtima wonse ansembewo. Masiku ano, Yehova akuseŵenzetsa Yesu Khristu waulemelelo monga Mkulu wa Ansembe wapamwamba. (Aheb. 9:11, 12) Mu 1919, Yesu anaika kagulu kocepa ka abale odzozedwa kukhala “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Kodi pali umboni wotani woonetsa kuti Yehova anamuvomeleza kapoloyu ndipo akumudalitsa na kum’cilikiza?

  • Olo kuti anthu a Mulungu akhala akuzunzidwa mosalekeza, kapolo wokhulupilika wapitiliza kupeleka cakudya cauzimu

  • Monga mmene ulosi unakambila, uthenga wabwino ukulalikidwa “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mat. 24:14

Kodi tingamucilikize bwanji kapolo wokhulupilika ndi wanzelu na mtima wonse?