Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Phunzitsani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu

Phunzitsani Maphunzilo Anu a Baibo Kudzidyetsa Okha Mwauzimu

Kuti ophunzila Baibo athetse njala yawo yauzimu na kupita patsogolo mwauzimu, ayenela kuphunzilanso zinthu zina kuwonjezela pa zimene timawaphunzitsa. (Mat. 5:3; Aheb. 5:12–6:2) Ayenelanso kuphunzila kudzidyetsa okha mwauzimu.

Mukangoyamba kuphunzila Baibo na munthu, muonetseni mmene angakonzekelele phunzilo la Baibo, ndipo m’limbikitseni kucita zimenezo. (mwb18.03 6) M’limbikitseni kuti azipemphela nthawi zonse asanayambe kukonzekela. Athandizeni ophunzila Baibo anu kupeza zida zophunzilila za pazipangizo, ndipo auzeni mmene angaziseŵenzetsele. Afotokozeleni mmene angapezele zofalitsa, mavidiyo, na zinthu zina zatsopano za pa jw.org na JW Broadcasting®. Mwapang’ono-pang’ono, aphunzitseni kuti aziŵelenga Baibo tsiku lililonse, kukonzekela misonkhano ya mpingo, na kudzifufuzila mayankho pa mafunso amene ali nawo. Alimbikitseni kuti azisinkhasinkha pa zimene amaphunzila.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI THANDIZANI MAPHUNZILO ANU A BAIBO KUDZIDYETSA OKHA MWAUZIMU, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi Neeta anam’thandiza bwanji Rose kuona kuti kuphunzila sikutanthauza kudziŵa cabe mayankho?

  • N’ciani cinathandiza Rose kumvetsa kuti Yehova anacita bwino kuletsa khalidwe laciwelewele?

  • Thandizani ophunzila anu kudziŵa coonadi komanso mmene ayenela kucigwilitsila nchito

    Kodi Rose anazindikila ciani pa nkhani ya kusinkhasinkha?