Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Timayamika Yehova Cifukwa ca Cikondi Canu

Timayamika Yehova Cifukwa ca Cikondi Canu

Akhristu a mu mpingo wa ku Tesalonika anaonetsa cikondi kwa Akhristu anzawo, ngakhale kuti nawonso anali kukumana na mavuto. (2 Ates. 1:3, 4) Masiku anonso, anthu a Yehova amaonetsa cikondi ngati cimeneco kwa abale na alongo padziko lonse lapansi. Nkhani za pa jw.org za mutu wakuti “Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito,” zimaonetsa mmene zopeleka zanu zimathandizila abale m’nthawi zovuta zino. Tikuyamikilani kaamba ka cikondi canu komanso cifukwa ca kucilikiza kwanu mowoloŵa manja.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI TIMAYAMIKA MULUNGU NTHAWI ZONSE CIFUKWA CA INU,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

• Kodi zopeleka zathu zimathandizilanso pa nchito zina ziti?

• Kodi njila yabwino kwambili yopelekela thandizo la ndalama kwa abale na alongo athu osoŵa ni iti?—Onaninso nkhani ya pa jw.org ya mutu wakuti “Zoculuka Zimathandizila pa Zimene Akusoŵa