November 22-28
OWERUZA 1-3
Nyimbo 126 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Nkhani Yocititsa Cidwi Yoonetsa Kulimba Mtima”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Ower. 2:10-12—N’cifukwa ciani zimenezi ni cenjezo kwa ife? (w05 1/15 24 ¶7)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Ower. 3:12-31 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
“Wonjezelani Cimwemwe Canu mu Ulaliki—Landilani Thandizo la Yehova Kupitila M’pemphelo”: (Mph. 10) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Pezani Cimwemwe pa Nchito Yopanga Ophunzila—Landilani Thandizo la Yehova—Pemphelo.
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lffi phunzilo 02 ndime yoyamba na mfundo 1-3 (th phunzilo 11)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khala Bwenzi la Yehova—Uzionetsa Khalidwe Labwino mu Ulaliki: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Ndiyeno ngati n’zotheka, pemphani ana amene munawasankhilatu kuti abwele ku pulatifomu na kuwafunsa mafunso awa: Tingakonzekele bwanji ulaliki? Kodi tingavale bwanji kuti maonekedwe athu akhale oyenela komanso osadzionetsela? Tingaonetse bwanji khalidwe labwino pamene tili mu ulaliki?
“Zimene Mungacite Kuti Kukumana Kotenga Malangizo a Ulaliki Kuzikhala Kopindulitsa”: (Mph. 10) Nkhani yokambilana, yokambidwa na woyang’anila utumiki. Pemphani omvetsela kuti afotokoze cifukwa cake tiyenela kufika mwamsanga pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb phunzilo 65
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 137 na Pemphelo