Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Zimene Mungacite Kuti Kukumana Kotenga Malangizo a Ulaliki Kuzikhala Kopindulitsa

Zimene Mungacite Kuti Kukumana Kotenga Malangizo a Ulaliki Kuzikhala Kopindulitsa

Mofanana na misonkhano ina yonse ya mpingo, kukumana kotenga malangizo a ulaliki ni msonkhano umene Yehova anatikonzela kuti tizilimbikitsana pa cikondi na nchito zabwino. (Aheb. 10:24, 25) Kukumanaku kuyenela kutenga mphindi 5 mpaka 7, kuphatikizapo nthawi yogaŵana, kugawa magawo, na kupemphela. (Ngati kukumanaku kwacitika pambuyo pa msonkhano, kuyenela kutenga nthawi yocepela pamenepa.) Wotsogoza ayenela kukonzekela mfundo zothandiza kwa amene adzayenda mu ulaliki pa tsikulo. Mwacitsanzo, pa Ciwelu zingakhale zothandiza kungokambilana zimene tinganene kwa mwininyumba mu ulaliki, cifukwa ambili opezekapo amakhala kuti sanapezeke pa kukumana kotenga malangizo a ulaliki mkati mwa mlunguwo. Kodi mfundo zina zopindulitsa zimene tingakambilane ni ziti?

  • Makambilano acitsanzo a mu Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu

  • Mmene tingagwilitsile nchito cocitika caposacedwa poyambitsa makambilano, kapena nkhani ya panyuzi imene yamveka

  • Mmene mungayankhile ngati mwininyumba wakamba mawu ofala kwanuko okanila ulaliki

  • Mmene mungayankhile munthu amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu, wokhulupilila cisanduliko, amene amakamba cinenelo cina, kapena amene ali m’cipembedzo cimene si cofala m’gawo lanu

  • Mmene tingaseŵenzetsele mbali inayake ya pa webusaiti ya jw.org, JW Laibulali, kapena Baibo

  • Mmene tingagwilitsile nchito cimodzi mwa zida za m’Thuboksi yathu

  • Mmene tingacitile ulaliki winawake, monga ulaliki wa pafoni, wa makalata, wapoyela, maulendo obwelelako, kapena maphunzilo a Baibo

  • Kukambilana malangizo okumbutsa za citetezo, kulolela, makhalidwe abwino, kuona anthu moyenela, kapena mfundo zina zofanana na zimenezi

  • Phunzilo kapena vidiyo yocokela m’bulosha yakuti Dzipelekeni pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa

  • Mmene mungalimbikitsile mnzanu amene mwayenda naye mu ulaliki kapena kum’thandiza

  • Lemba lokamba za ulaliki, kapena cocitika colimbikitsa ca mu ulaliki