UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Mapemphelo Athu ni Amtengo Wapatali kwa Yehova
Mapemphelo ovomelezeka ali monga zofukiza zonunkhila zimene zinali kutenthedwa pamaso pa Yehova nthawi zonse pa kacisi. (Sal. 141:2) Timaonetsa kuti timaona ubale wathu na Atate wathu wakumwamba kukhala wamtengo wapatali mwa kumuuza mmene timam’kondela, kumuyamikila, kumufotokozela nkhawa na zolakalaka zathu, na kumupempha kuti atitsogolele mu umoyo wathu. Mosakayikila, Yehova amaona mapemphelo athu acidule a kumisonkhano kukhala ofunika kwambili pa kulambila kwathu. Komabe, Yehova ayenela kuti amakondwela kwambili ngati pa mapemphelo athu a munthu mwini timamuuza za mumtima mwathu na kukambilana naye kwa nthawi yotalikilapo!—Miy. 15:8.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI NIMAKONDA KWAMBILI KUPEMPHELA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Kodi M’bale Johnson anakhalako na mwayi wocita mautumiki otani?
-
Kodi iye anaonetsa bwanji kudalila Yehova m’mapemphelo ake?
-
Kodi mwaphunzilapo ciyani pa zocitika za mu umoyo wa M’bale Johnson?