UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yehova Saiŵala Nchito Yathu Imene Timagwila Molimbika
Nthawi zina, tingaone kuti nchito imene timagwila molimbika pothandiza ena, anthuwo saiyamikila komanso amaiiŵala mwamsanga. Nanga bwanji nchito imene timacita potumikila Yehova? Kodi iye amaiona bwanji? Mulungu wathu ni woyamikila, ndipo saiŵala kudzipeleka kwathu pom’tumikila. Ngakhale kuti sitingacite zambili mmene tinali kucitila kale cifukwa ca kufooka kwa thanzi, Yehova sadzatisiya.—Aheb. 6:10.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA SAIŴALA. KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi M’bale Hibshman anagwila bwanji nchito molimbika potumikila Yehova m’mautumiki osiyanasiyana?
-
Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti sanamuiŵale m’bale Hibshman mkazi wake atamwalila, komanso pamene sanali kucita zambili ngati kale cifukwa ca ukalamba?
-
N’cifukwa ciyani tingakambe kuti umoyo wa mu utumiki wa nthawi zonse wa M’bale Hibshman wamupindulila kwambili?—Miy. 10:22