CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Nyumba Yonse ya Ahabu Idzafafanizidwa”—2 Maf. 9:8
UFUMU WA YUDA
Yehosafati ni mfumu
ca m’ma 911: Yehoramu (mwana wa Yehosafati, mwamuna wa Ataliya, amene anali mwana wamkazi wa Ahabu na Yezebeli) anayamba kulamulila yekha monga mfumu
ca m’ma 906: Ahaziya (mdzukulu wa Ahabu na Yezebeli) anakhala mfumu
ca m’ma 905: Ataliya anapha ana onse acifumu na kulanda ufumu. M’dzukulu wake Yehoasi ndiye yekha anapulumuka ndipo anabisidwa na Mkulu wa Ansembe Yehoyada.—2 Maf. 11:1-3
ca m’ma 898: Yehoasi anakhala mfumu. Mfumukazi Ataliya anaphedwa na Mkulu wa Ansembe Yehoyada. —2 Maf. 11:4-16
UFUMU WA ISIRAELI
ca m’ma 920: Ahaziya (mwana wa Ahabu na Yezebeli) anakhala mfumu
ca m’ma 917: Yehoramu (mwana wa Ahabu na Yezebeli) anakhala mfumu
ca m’ma 905: Yehu anapha Mfumu Yehoramu ya Isiraeli na abale ake. Anaphanso amayi ake a Yehoramu (Yezebeli) komanso mfumu Ahaziya ya Yuda na abale ake.—2 Maf. 9:14–10:17
ca m’ma 904: Yehu anayamba kulamulila monga mfumu