November 20-26
YOBU 18-19
Nyimbo 44 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musawasiye Konse Alambili Anzanu”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Yobu 19:1, 2—Tiphunzilapo ciyani tikaganizila yankho limene Yobu anapeleka “anzake” atamulankhula mawu ankhanza? (w94 10/1 32)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo iti yokupindulilani imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Yobu 18:1-21 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. Mukayamba, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 12)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. Itanilani munthuyo ku misonkhano. Chulani na kukambilanako vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu? (Koma musaitambitse) (th phunzilo 3)
Nkhani: (Mph. 5) w20.10 17 ¶10-11—Mutu: Limbikitsani Maphunzilo Anu Kupeza Mabwenzi mu Mpingo. (th phunzilo 20)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khala Bwenzi la Yehova—Thandizani Ena: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Ndiyeno ngati n’kotheka, funsani mafunso ana amene munaŵasankhilatu. Afunseni kuti: Inu ana kodi mungaŵathandize bwanji ena?
Kodi ungakonde kucita ciyani kuti uthandize ena?
“Makonzedwe Olimbikitsa Atumiki a pa Beteli”: (Mph. 10) Kukambilana na kutamba vidiyo.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) bt mutu. 2 ¶8-15
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 63 na Pemphelo