Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Munthu Akafa, Kodi Angakhalenso Ndi Moyo?

Munthu Akafa, Kodi Angakhalenso Ndi Moyo?

Palibe munthu angathaŵe imfa kapena kuukitsa akufa (Yobu 14:​1, 2, 4, 10; w99 10/15 3 ¶1-3)

Akufa angakhalenso na moyo (Yobu 14:​7-9; w15 4/15 32 ¶1-2)

Yehova ali na mphamvu zoukitsa atumiki ake, ndipo amacita kulakalaka kutelo (Yobu 14:​14, 15; w11 3/1 22 ¶5)

ZOYENELA KUZISINKHASINKHA: N’cifukwa ciyani Yehova amacita kulakalaka kuti adzaukitse atumiki ake okhulupilika? Kodi izi zimakucititsani kumuona bwanji Yehova?