Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

‘Muziika Kenakake Pambali’

‘Muziika Kenakake Pambali’

Tiyenela kucita zopeleka mwaufulu nthawi zonse. Izi n’zimene mtumwi Paulo anatilimbikitsa kucita pamene anati, ‘muziika kenakake pambali.’ (1 Akor. 16:2) Kutsatila malangizo ouzilidwa amenewa kumatithandiza kupititsa patsogolo kulambila koyela, ndipo kumatibweletsela cimwemwe. Mwina tingaone kuti zopeleka zathu n’zocepa kwambili. Koma Yehova amayamikila ngako kuona kuti ndife ofunitsitsa kumulemekeza na zinthu zathu zamtengo wapatali.—Miy. 3:9.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI TIKUYAMIKILANI CIFUKWA COIKA KENAKAKE PAMBALI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi pamakhala mapindu otani tikamakonzelatu zopeleka zathu?

  • Kodi ena amacita ciyani kuti ‘aziika kenakake pambali’?