Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

November 4-10

SALIMO 105

November 4-10

Nyimbo 3 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Amakumbukila Pangano Lake Mpaka Kalekale”

(Mph. 10)

Yehova anacita pangano lake na Abulahamu, ndipo analibwelezanso kwa Isaki komanso Yakobo (Gen. 15:18; 26:3; 28:13; Sal. 105:​8-11)

Kukwanilitsidwa kwa lonjezo limeneli kunaoneka ngati kosatheka (Sal. 105:​12, 13; w23.04 28 ¶11-12)

Yehova sanaiŵale lonjezo lake kwa Abulahamu (Sal. 105:​42-44; it-2-E 1201 ¶2)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kudalilika kwa Yehova kumanilimbikitsa bwanji?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 105:​17-19—Kodi “mawu a Yehova” anamuyenga motani Yosefe? (w86-CN 11/1 19 ¶15)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 105:​24-45 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 1) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwininyumba ni wotangwanika. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Thetsani makambilano anu mwaubwenzi pamene mwininyumba wayambitsa mkangano (lmd phunzilo 4 mfundo 5)

6. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Gaŵilani magazini yokhala na nkhani imene mwininyumba anacita nayo cidwi pa ulendo wapita. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)

7. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Muuzeni za JW Laibulale® ndipo muthandizeni kuicita daunilodi. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 84

8. Mmene Mungaonetsele Kuti Mumam’konda Yesu

(Mph. 15) Kukambilana.

Tikamaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso cuma cathu popititsa patsogolo nchito ya Ufumu, timaonetsa kuti timaikonda Mfumu yathu Khristu Yesu. Kucita zimenezi kumakondweletsa Yehova komanso abale na alongo athu. (Yoh. 14:23) Nkhani za pa jw.org zakuti “Mmene Zopeleka Zanu Zimagwilila Nchito” zimaonetsa mmene zopeleka zathu zimathandizila kwambili abale na alongo padziko lonse.

Tambitsani VIDIYO yakuti Zopeleka Zanu Zimagwila Nchito Yaikulu. Kenako funsani omvela kuti:

  • Nthawi zina zopeleka zimagwilitsidwa nchito pomenyela ufulu wathu wa kulambila. Kodi izi zawathandiza bwanji abale athu?

  • Kodi kuonetsetsa kuti pali “kufanana” pa kagwilitsidwe nchito ka zopeleka kwathandiza bwanji pomanga Nyumba za Ufumu?—2 Akor. 8:14

  • Kodi pakhala mapindu otani cifukwa coseŵenzetsa zopeleka pomasulila Baibo m’zinenelo zambili?

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 17 ¶13-19

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 97 na Pemphelo