December 23-29
SALIMO 119:121-176
Nyimbo 31 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Mmene Tingapewele Kudzibweletsela Zopweteka
(Mph. 10)
Muzikonda malamulo a Mulungu (Sal. 119:127; w18.06 17 ¶5-6)
Muzidana na zoipa (Sal. 119:128; w93-CN 4/15 17 ¶12)
Mvelani Yehova kuti mupewe kulakwitsa zinthu ngati mmene anthu ‘osadziŵa zambili’ amacitila (Sal. 119:130, 133; Miy. 22:3)
DZIFUNSENI KUTI, ‘N’zinthu ziti zimene niyenela kuwongolela poonetsa kuti nimakonda kwambili malamulo a Mulungu kapena kudana na zoipa?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Sal. 119:160—Malinga na vesili, kodi tiyenela kukhala otsimikiza za ciyani? (w23.01 2 ¶2)
-
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 119:121-152 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA (lmd phunzilo 1 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA Muonetseni mopezela nkhani imene ingamucititse cidwi pa jw.org. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) Kambilanani na wophunzila Baibo amene sapezeka pa misonkhano ya mpingo kaŵili-kaŵili. (lmd phunzilo 12 mfundo 4)
Nyimbo 121
7. Musadzibweletsele Zopweteka Cifukwa Cokonda Ndalama
(Mph. 15) Kukambilana.
Anthu amene amakonda ndalama “adzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.” (1 Tim. 6:9, 10) Pansipa pandandalikidwa mavuto amene tingakumane nawo ngati timakonda ndalama komanso ngati timaziona kuti ndizo zofunika ngako pa moyo wathu.
-
Sitingakhale paubale wolimba na Yehova. —Mat. 6:24
-
Sitidzakhala wokhutila.—Mlal. 5:10
-
Cingakhale covuta kupewa makhalidwe oipa monga kunama, kuba, komanso cinyengo. (Miy. 28:20) Izi zingapangitse kuti cikumbumtima cathu cizitivutitsa, ndiponso tingawononge mbili yathu komanso ubwenzi wathu na Yehova
Ŵelengani Aheberi 13:5, kenako kambilanani funso ili:
-
Kodi ndalama tiyenela kuziona bwanji kuti tipewe zopweteka? Nanga n’cifukwa ciyani?
Ngakhale kuti sitikonda ndalama, tingakumanebe na zopweteka ngati sitizigwilitsa nchito mwanzelu.
Tambitsani vidiyo ya TUKADOLI TOJAMBULA PAMANJA Yakuti Mmene Mungaseŵenzetsele Ndalama Zanu. Kenako funsani omvela mafunso awa:
-
N’cifukwa ciyani tiyenela kupanga bajeti? Nanga tingacite bwanji zimenezi?
-
N’cifukwa ciyani ni bwino kumasungako ndalama?
-
N’cifukwa ciyani tiyenela kupewa nkhongole zosafunikila?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 20 ¶1-7, komanso mawu oyamba a cigawo 7