December 30, 2024–January 5, 2025
MASALIMO 120-126
Nyimbo 144 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Anabyala Akulila, koma Anakolola Akusangalala
(Mph. 10)
Aisiraeli anasangalala atamasulidwa ku ukapolo ku Babulo kuti akabwezeletse kulambila koona (Sal. 126:1-3)
Aisiraeli amene anabwelela ku Yudeya analila, mwina cifukwa ca kukula kwa nchito imene anafunika kugwila (Sal. 126:5; w04-CN 6/1 16 ¶10)
Koma iwo analimbikila kugwila nchitoyo ndipo anadalitsidwa (Sal. 126:6; w21.11 24 ¶17; w01-CN 7/15 18-19 ¶13-14; onani cithunzi )
ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: Pambuyo populumutsidwa pa nkhondo ya Aramagedo, kodi n’zovuta ziti zimene tidzakumana nazo pokonzanso dzikoli? Nanga tidzapeza madalitso otani?
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Sal. 124:2-5—Kodi tiyenela kuyembekezela kuti Yehova adzateteza moyo wathu ngati mmene anacitila kwa Aisiraeli? (cl-CN 73 ¶15)
-
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 124:1–126:6 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Pa makambilano apita, munthuyo anaonetsa kuti sakhulupilila Baibo. (lmd phunzilo 9 mfundo 5)
6. Kupanga Ophunzila
Nyimbo 155
7. Kondwelani na Malonjezo a Mulungu
(Mph. 15.) Kukambilana.
Yehova anakwanilitsa zimene analonjeza kwa anthu amene anagwidwa ukapolo ku Babulo. Anawapulumutsa na kuwacilitsa mwauzimu. (Yes. 33:24) Iye anateteza anthuwo komanso ziweto zawo ku mikango yolusa komanso zilombo zina zimene zinali zitaculuka pa nthawiyo. (Yes. 65:25) Iwo anali kukhala m’nyumba zawo-zawo komanso kudya zipatso za m’minda yawo ya mpesa. (Yes. 65:21) Mulungu anadalitsa nchito yawo, ndipo iwo anakhala na moyo wautali.—Yes. 65:22, 23.
Tambitsani VIDIYO Yakuti Kondwelani na Malonjezo a Mulungu Okamba za Mtendele—Mbali Yake. Ndiyeno funsani omvela kuti:
-
Kodi maulosi amenewa akukwanilitsika motani masiku ano?
-
Nanga adzakwanilitsika motani pa mlingo waukulu m’dziko latsopano?
-
Kodi ni ulosi uti umene inu mukuuyembekezela mwacidwi?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 20 ¶8-12, bokosi pa tsa. 161