December 9-15
SALIMO 119:1-56
Nyimbo 124 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. “Kodi Wacinyamata Angakhale Bwanji Woyela pa Moyo Wake?”
(Mph. 10)
Khalani osamala nthawi zonse pa zocita zanu (Sal. 119:9; w87-CN 11/1 18 ¶10)
Muziyesetsa kutsatila zikumbutso za Mulungu (Sal. 119:24, 31, 36; w06 6/15 25 ¶1)
Pewani kuyang’ana zinthu zopanda pake (Sal. 119:37; w10-CN 4/15 20 ¶2)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ni zikumbutso ziti zimene nalandila zonithandiza kukhalabe woyela?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 119—Kodi salimoli linalembedwa m’njila yotani? Nanga n’cifukwa ciyani linalembedwa m’njila imeneyi? (w05-CN 4/15 10 ¶2)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 119:1-32 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Yambitsani makambilano na munthu amene mwakumana naye m’njila pocita ulaliki wa nyumba na nyumba. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo anakuuzani kuti posacedwa anatayikilidwa wokondedwa wake mu imfa. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwyp 83—Mutu: Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa? (th phunzilo 20)
Nyimbo 40
7. Vidiyo yakuti Zimene Gulu Lakwanitsa Kucita ya December
(Mph. 10) Tambitsani VIDIYO.
8. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 5)
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 19 ¶6-13