Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

November 18-24

MASALIMO 107-108

November 18-24

Nyimbo 7 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Yamikani Yehova Cifukwa Iye Ndi Wabwino”

(Mph. 10)

Monga mmene Yehova anapulumutsila Aisiraeli mu ukapolo ku Babulo, iye watipulumutsa m’dziko la Satanali (Sal. 107:​1, 2; Akol. 1:​13, 14)

Kuyamikila Yehova kumatilimbikitsa kum’tamanda mu mpingo (Sal. 107:​31, 32; w07-CN 4/15 20 ¶2)

Tingakulitse ciyamikilo cathu pa Yehova mwa kuganizila zabwino zimene waticitila (Sal. 107:43; w15 1/15 9 ¶4)

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 108:9—Kodi mawu akuti “Mowabu ndi beseni langa losambilamo,” ayenela kuti atanthauza ciyani? (it-2-E 420 ¶4)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 107:​1-28 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Muuzeni za pulogilamu yathu yophunzitsa Baibo na kumusiyila kakhadi kopemphela phunzilo la Baibo. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) ijwyp 90—Mutu: Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika? (th phunzilo 14)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 46

7. Timaimba Nyimbo Kuti Tiyamikile Yehova

(Mph. 15) Kukambilana.

Yehova atapulumutsa Aisiraeli kwa asilikali amphamvu a Iguputo pa Nyanja Yofiila, Aisiraeliwo anamuyamikila kwambili moti anamuimbila nyimbo. (Eks. 15:​1-19) Amuna ndiwo anatsogolela poimba nyimbo yatsopano imeneyo. (Eks. 15:21) Nayenso Yesu komanso Akhristu oyambilila, anali kuimba nyimbo zotamanda Mulungu. (Mat. 26:30; Akol. 3:16) Ifenso masiku ano timatamanda Yehova mwa kuimba nyimbo pa misonkhano ya mpingo, ya dela, komanso ya cigawo. Mwacitsanzo, nyimbo imene tangoimba kumene yakuti, “Tikuyamikani Yehova,” yakhala ikuimbidwa pa misonkhano yathu kuyambila mu 1966.

M’madela ena, amuna amacita manyazi kuimba nyimbo pa gulu. Koma tizikumbukila kuti kuimba pa misonkhano ni mbali ya kulambila kwathu. Pamakhala nchito yaikulu kuti gulu la Yehova lipange nyimbo zomveka bwino, komanso kuti lisankhe nyimbo zogwilizana na msonkhano ulionse. Ife mbali yathu ni yosavuta. Timangofunika kuimbila pamodzi nyimbozi poonetsa cikondi na ciyamikilo cathu cocokela pansi pa mtima kwa Atate wathu wakumwamba.

Tambitsani VIDIYO yakuti Mbili ya Kupita Patsogolo Kwa Gulu Lathu—Mphatso ya Nyimbo, Gawo 2. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi n’cocitika cosaiŵalika citi cimene cinacitika mu 1944?

  • Kodi abale athu ku Siberia anaonetsa bwanji kuti anali kukonda kuimba nyimbo za Ufumu?

  • N’cifukwa ciyani ife Mboni za Yehova timaona kuti kuimba nyimbo n’kofunika kwambili?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 18 ¶6-15

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 73 na Pemphelo