November 25–December 1
MASALIMO 109-112
Nyimbo 14 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Thandizilani Yesu Amene ni Mfumu!
(Mph. 10)
Yesu atabwelela kumwamba, anakhala ku dzanja lamanja la Yehova (Sal. 110:1; w06-CN 9/1 13 ¶6)
Mu 1914, Yesu anayamba kugonjetsa adani ake (Sal. 110:2; w00-CN 4/1 18 ¶3)
Tiyenela kudzipeleka na mtima wonse pothandizila ulamulilo wa Yesu (Sal. 110:3; be 76 ¶2)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi n’zolinga ziti zimene ningadziikile zoonetsa kuti nikuthandiza pa nchito ya Ufumu?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Sal. 110:4—Fotokozani pangano lochulidwa pa vesili. (it-1-E 524 ¶2)
-
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 109:1-26 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Seŵenzetsani thilakiti poyambitsa makambilano. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)
5. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq 23—Mutu: N’chifukwa Chiyani Simupita Kunkhondo? (lmd phunzilo 4 mfundo 4)
6. Kupanga Ophunzila
Nyimbo 72
7. Tingacite Ciyani Pocilikiza Ufumu Mokhulupilika?
(Mph. 15) Kukambilana.
Ufumu wa Yehova ni njila imene iye amaonetsela mphamvu zake monga Wolamulila wa cilengedwe conse. (Dan. 2:44, 45) Conco, tikamayesetsa kucita zinthu zoonetsa kuti tili ku mbali ya Ufumu wa Mulungu, timasonyeza kuti timakhulupilila kuti Yehova ndiye wolamulila wabwino koposa.
Tambitsani VIDIYO Yakuti Thandizilani “Kalonga Wamtendele” Mokhulupilika. Ndiyeno funsani omvela kuti:
-
Kodi ni motani mmene timathandizila Ufumu wa Mulungu mokhulupilika?
Lembani lemba logwilizana na mfundo iliyonse pansipa poonetsa mmene tingakhalile ku mbali ya Ufumu wa Mulungu.
-
Kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu.
-
Kutsatila mfundo za makhalidwe abwino zimene nzika za Ufumu ziyenela kutsatila.
-
Kulalikila mwakhama uthenga wa Ufumu.
-
Kuonetsa ulemu kwa olamulila a boma, kwinaku tikumvela Mulungu ngati malamulo a Kaisara akutsutsana na malamulo a Mulungu.
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 18 ¶16-24