UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO October 2016
Maulaliki a Citsanzo
Maulaliki a citsanzo osewenzetsa pogaŵila Galamukani!, kapepa koitanila ku misonkhano, ndi Mfundo ya coonadi ca m’Baibo yokamba zimene zimacitika munthu akafa. Konzani ulaliki wanu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khulupilila Yehova ndi Mtima Wako Wonse”
Lemba la Miyambo 3 limatitsimikizila kuti Yehova Mulungu adzatidalitsa ngati timam’khulupilila. Mungadziŵe bwanji kuti mumakhulupilila Yehova na mtima wanu wonse?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Mtima Wako Usapatuke”
Lemba la Miyambo 7 likamba za mmene mnyamata wina anakopedwela mpaka kufika pocita chimo cifukwa conyalanyaza mfundo za Yehova. Tingaphunzilepo ciani pa zolakwa zake?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Nzelu ni Zabwino Kwambili Kuposa Golide
Lemba la Miyambo 16 limakamba kuti ndi bwino kupeza nzelu kuposa golide. N’cifukwa ciani nzelu yocokela kwa Mulungu ni yamtengo wapatali?
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Mmene Mungapelekele Mayankho Ogwila Mtima
Yankho labwino limapindulitsa mpingo ndi munthu woyankhayo. Kodi yankho labwino limakhala labwanji?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Muziyesetsa Kukhala Mwamtendele na Ena
Anthu a Yehova amacita khama kuti akhale pa mtendele na anzawo. Tingaseŵenzetse Mau a Mulungu kuti atithandize kubweza mkwiyo na kukhazikitsa mtendele.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Phunzitsa Mwana m’Njila Yomuyenelela”
N’cifukwa ciani cilango n’cofunika kuti makolo aphunzitse bwino ana? Pa Miyambo 22 pali malangizo othandiza kwa makolo.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Kodi Mumaseŵenzetsa Makadi Ongenela pa Webusati Yathu?
Muziseŵenzetsa makadi amenewa pa mpata uliwonse kuti muthandize anthu kucita cidwi na Mau a Mulungu ndi webusaiti yathu.