October 3-9
MIYAMBO 1–6
Nyimbo 37 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Khulupilila Yehova Ndi Mtima Wako Wonse”: (Mph. 10)
[Onetsani vidiyo ya Mfundo Zokhudza Buku la Miyambo.]
Miy. 3:1-4—Khalani wokoma mtima ndi wokhulupilika (w00 1/15 CN, tsa. 23-24)
Miy. 3:5-8—Muziyesetsa kudalila Yehova ndi mtima wonse (w00 1/15 24)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Miy. 1:7—Kodi kuopa Yehova ndi “ciyambi ca kudziŵa zinthu” m’njila yotani? (w06 9/15-CN, tsa. 17 ndime 1; it-2 180)
Miy. 6:1-5—N’ciani canzelu cimene muyenela kucita ngati mwaloŵa m’pangano losayenela la zamalonda? (w00 9/15 CN, tsa 25-26)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Miy. 6: 20-35
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani mavidiyo a maulaliki acitsanzo, ndipo kambilanani mfundo zake. Limbikitsani ofalitsa kutengako mbali mokwanila pa nchito ya padziko lonse yoitanila anthu ku misonkhano ya kumapeto kwa mlungu.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Zosoŵa za Pampingo: (Mph. 8) Ngati mufuna, kambilanani mfundo zimene mwaphunzila mu Buku Lapacaka (yb16, tsa 25-27)
Muzicitila Zabwino Anthu Amene Amapezeka pa Misonkhano Yathu (Miy. 3:27) : (Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti N’ciani Cimacitika ku Nyumba ya Ufumu?. Ngati vidiyo kulibe, kambilanani phunzilo 7 m’kabuku kakuti Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? Ndiyeno funsani ofalitsa kuti afotokoze mmene tingalimbikitsile mzimu wa cikondi pa Nyumba ya Ufumu, nthawi zonse, osati cabe m’mwezi wa October.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) kr nkhani 2 ndime 1-12
Kubwelelamo na Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 143 na Pemphelo