MIYAMBO 1–6
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |“Khulupilila Yehova ndi Mtima Wako Wonse”
Yehova ni woyenela kumukhulupilila ndi mtima wonse. Tanthauzo la dzina lake limatipangitsa kukhulupilila kuti adzakwanilitsa malonjezo ake onse. Pemphelo limatithandiza kwambili kukhulupilila Mulungu. Miyambo caputa 3 imatitsimikizila kuti, ngati ndife okhulupilika kwa Yehova, iye adzatidalitsa mwa ‘kuwongola njila zathu.’
Munthu amene amadziona kuti ni wanzelu . . .
3:5-7
-
amasankha zocita asanapemphe Yehova kuti amutsogolele
-
amadalila nzelu zake kapena za dziko
Munthu amene amakhulupilila Yehova . . .
-
amayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu mwa kuphunzila Baibo, kusinkha-sinkha, ndi kupemphela
-
amafuna-funa citsogozo ca Mulungu mwa kufufuza mfundo za m’Baibo pamene asankha zocita
COYAMBA: Nimasankha zimene naona kuti ndiye zoyenela |
COYAMBA: Nimapempha citsogozo ca Yehova kupitila m’pemphelo ndi phunzilo laumwini |
CACIŴILI: Nimapempha Yehova kuti adalitse zimene nasankha |
CACIŴILI: Nimapanga zosankha zogwilizana na mfundo za m’Baibo |