October 10-16
MIYAMBO 7–11
Nyimbo 32 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Mtima Wako Usapatuke” (Mph. 10)
Miy. 7:6-12—Anthu opanda nzelu mumtima mwawo amawononga umoyo wawo wauzimu (w00 11/15 CN, tsa 29-30)
Miy. 7:13-23—Kusankha zocita mopanda nzelu kumabweletsa mavuto (w00 11/15 CN, tsa. 30-31)
Miy. 7:4, 5, 24-27—Nzelu ndi kumvetsa zinthu kumatiteteza (w00 11/15 CN, tsa. 29, 31)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Miy. 9:7-9—Kodi zimene timacita tikapatsidwa uphungu zimaonetsa kuti ndife anthu a bwanji? (w01 5/15-CN, tsa. 29-30)
Miy. 10:22—Ndi madalitso a Yehova ati amene timalandila masiku ano? (w06 5/15 CN, tsa. 26-30 ndime 3-16)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Miy. 8:22–9:6
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) bh tsa. 176 ndime 5-6—Itanilani wophunzilayo ku misonkhano.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
Zimene Acicepele Anzanu Amakamba—Mafoni (Miy. 10:19): (Mphi. 15) Kukambilana. Yambani mwa kutambitsa vidiyo yakuti Zimene Acicepele Anzanu Amakamba—Mafoni, ngati ilipo. Ndiyeno kambilanani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Mameseji a Pafoni?” Nkhaniyi mungaipeze pa webusaiti m’Chichewa. Gogomezani mfundo zimene zili pa kamutu kakuti “Zofunika kukumbukira pa nkhani ya mameseji.”
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) kr nkhani 2 ndime 13-22
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 152 na Pemphelo
Cikumbutso: Lizani nyimboyi kamodzi, pambuyo pake mpingo wonse uyimbile pamodzi