October 17-23
MIYAMBO 12–16
Nyimbo 69 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Nzelu ni Yabwino Kwambili Kuposa Golide”: (Mph. 10)
Miy. 16:16, 17—Munthu wanzelu amaphunzila Mau a Mulungu ndi kuwaseŵenzetsa (w07 7/15 CN, tsa 8)
Miy. 16:18, 19—Munthu wanzelu amapewa kunyada ndi kudzikuza (w07 7/15 CN, tsa. 8-9)
Miy. 16:20-24—Munthu wanzelu amakamba mau olimbikitsa kwa ena (w07 7/15 CN, tsa. 9-10)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Miy. 15:15—Tingacite ciani kuti tizikhala osangalala kwambili pa umoyo wathu? (g 11/13 tsa. 16)
Miy. 16:4—Kodi mfundo yakuti Yehova anapanga oipa “n’colinga” itanthauza ciani? (w07 5/15-CN, tsa. 18-19)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Miy. 15:18 mpaka 16:6
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Yoh. 11:11-14—Phunzitsani Coonadi. Itanilani munthuyo ku misonkhano ya kumapeto kwa mlungu.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Gen. 3: 1-6; Aroma 5: 12—Phunzitsani Coonadi. Itanilani munthuyo ku misonkhano ya kumapeto kwa mlungu.
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) bh tsa, 191 ndime 18-19—Itanilani wophunzilayo ku misonkhano.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
“Mmene Mungapelekele Mayankho Ogwila Mtima”: (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Khala Bwenzi la Yehova—Konzekela Yankho Lako. Ndiyeno itanani ana ocepa kuti abwele ku pulatifomu ndipo afunseni kuti: N’zinthu zinai ziti zimene tiyenela kucita pokonzekela mayankho athu? N’cifukwa ciani sitiyenela kukhumudwa ngati sitinapatsidwe mwayi woyankha pa misonkhano?
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) kr mutu 2 ndime 23-34
Kubwelelamo na Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 102 na Pemphelo