Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MIYAMBO 12–16

Nzelu ni Zabwino Kwambili Kuposa Golide

Nzelu ni Zabwino Kwambili Kuposa Golide

N’cifukwa ciani nzelu zocokela kwa Mulungu ni zapamwamba? Zimathandiza munthu kupewa njila zoipa na kusunga moyo wake. Zimamuthandizanso kukhala na maganizo abwino, kukamba zabwino ndi kucita zabwino.

Nzelu zimatithandiza kupewa kunyada

16:18, 19

  • Munthu wanzelu amadziwa kuti Yehova ndiye Gwelo la nzelu zonse

  • Anthu amene acita zinthu zapamwamba kapena amene apatsidwa maudindo, afunika kupewa kunyada ndi kudzikuza

Nzelu zimalimbikitsa munthu kukamba mau abwino

16:21-24

  • Munthu wanzelu amayesetsa kuona zabwino mwa ena ndi kukamba zabwino zokhudza iwo

  • Mau anzelu amakhala okopa ndi okoma ngati uci, osati aukali kapena a mikangano