October 31–November 6
MIYAMBO 22-26
Nyimbo 88 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Phunzitsa Mwana M’njila Yomuyenelela”: (Mph. 10)
Miy. 22:6; 23:24, 25—Kuphunzitsa ana m’njila ya Mulungu, kumawathandiza kukhala osangalala ndi odalilika akadzakula (w08 4/1-CN, tsa. 16; w07 6/1-CN, tsa. 31)
Miy. 22:15; 23:13, 14—M’banja, “ndodo” itanthauza mitundu yonse ya cilango coyenelela (w97 10/15-CN, tsa. 32; it-2 818 ndime 4)
Miy. 23:22—Acicepele angapindule na malangizo anzelu a makolo awo (w04 6/15-CN, tsa. 14 ndime 1-3; w00 6/15-CN, tsa. 21 ndime 13)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Miy. 24:16—Kodi mwambi uwu umatilimbikitsa bwanji kupilila pamene tili pa mpikisano wopita ku moyo? (w13 3/15-CN, masa. 4-5 ndime 5-8)
Miy. 24:27—Kodi mwambi uwu utanthauza ciani? (w09 10/15-CN, tsa. 12)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Miy. 22:1-21
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 2 kapena zocepelapo) Khadi yongenela pa Webusaiti yathu—Ulaliki wamwayi.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Khadi yongenela pa Webusaiti yathu—Yalani maziko a ulendo wobwelelako, ndipo tsilizani mwa kukamba mau oonetsa kuti mufuna kutambitsa mwininyumba vidiyo yakuti, N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo?
Phunzilo la Baibulo: (Mph. 6 kapena zocepelapo) lv masa. 179-181 ndime 18-19
UMOYO WATHU WA CIKHIRISTU
“Kodi Mumaseŵenzetsa Makadi Ongenela pa Webusaiti Yathu?”: (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani vidiyo ya ulaliki wacitsanzo. Ngati vidiyo kulibe, onetsani citsanzo ca mmene tingagaŵile khadi yongenela pa Webusaiti yathu. Ndiyeno kambilanani zimene mwaphunzilapo. Limbikitsani ofalitsa kuti azinyamulako makadi amenewa nthawi zonse.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) kr nkhani 3 ndime 1-12, masa. 30-31
Kubwelelamo na Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 146 na Pemphelo
Cikumbutso: Lizani nyimboyi kamodzi, pambuyo pake mpingo wonse uyimbile pamodzi.