UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO October 2018
Makambilano Acitsanzo
Makambilano otsatizana-tsatizana ofotokoza cifukwa cake anthu amavutika na zimene Mulungu adzacita pa mavutowo
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Yesu Amasamalila Nkhosa Zake
Yesu, amene ni M’busa wabwino, amadziŵa nkhosa iliyonse payokha—zimene imasoŵeka, zofooka zake, komanso mphamvu zake.
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Tengelani Cifundo ca Yesu
N’cifukwa ciani cifundo ca Yesu na kukoma mtima kwake kunali kocititsa cidwi?
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndakupatsani Citsanzo”
Yesu anaphunzitsa atumwi ake kuti afunika kukhala odzicepetsa komanso okonzeka kugwila nchito zotsika potumikila ena.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Pewani Kunyada na Mkwiyo
Kuti tionetse cikondi monga ca Khristu, tifunika kuika zofuna za ena patsogolo na kupewa kukwiya.
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Simuli Mbali ya Dzikoli”
Otsatila a Yesu afunika kukhala olimba mtima kuti asadetsedwe na anthu owazungulila.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela
Kuti tikhale ogwilizana, tifunika kuona zabwino mwa ena komanso kuwakhululukila na mtima wonse.
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Yesu Anacitila Umboni Coonadi
Pokhala ophunzila a Yesu, na ise timacitila umboni coonadi m’mawu na m’zocita.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kondwelani na Coonadi
Tifunika kucitila umboni coonadi komanso kumakamba zoona olo kuti tikukhala m’dziko lodzala mabodza ndiponso limene limacita zosalungama.