October 15-21
YOHANE 13-14
Nyimbo 100 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Ndakupatsani Citsanzo”: (10 min.)
Yoh. 13:5—Yesu anasambika mapazi a ophunzila ake (“kusambitsa mapazi a ophunzila” nwtsty mfundo younikila)
Yoh. 13:12-14—Ophunzila ake ndiwo anali na udindo ‘wosambikana mapazi’ (“muyenela” nwtsty mfundo younikila)
Yoh. 13:15—Ophunzila onse a Yesu afunika kutengela citsanzo cake ca kudzicepetsa (w99 3/1 peji 31 pala. 1)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yoh. 14:6—Kodi Yesu ni “njila, coonadi ndi moyo” m’lingalilo lanji? (“Ine ndine njila, coonadi ndi moyo” nwtsty mfundo younikila)
Yoh. 14:12—Kodi amene amakhulupilila mwa Yesu ‘amacita nchito zazikulu kuposa’ zake motani? (“nchito zazikulu kuposa zimenezi” nwtsty mfundo younikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Yoh. 13:1-17
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo pamene mucita ulaliki wamwayi.
Kubwelelako Koyamba: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo.
Vidiyo ya Kubwelelako Kaciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Pewani Kunyada ndi Kucita Zosayenela”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti “Muzikondana”—Pewani Kunyada ndi Kucita Zosayenela. Ngati nthawi ilola, kambilanani kabokosi kakuti “Citsanzo ca m’Baibo Cofunika Kucisinkha-sinkha.”
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu. 39
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 120 na Pemphelo