Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Pewani Kunyada na Mkwiyo

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Pewani Kunyada na Mkwiyo

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Yesu anaphunzitsa kuti ophunzila ake adzadziŵika cifukwa ca cikondi. (Yoh. 13:34, 35) Kuti tionetse cikondi monga ca Khristu, tifunika kuika zofuna za ena patsogolo na kupewa kukwiya. —1 Akor. 13:5.

MMENE TINGACITILE:

  • Ngati munthu wina wakamba kapena kucita zokukwiyitsani, yambani mwaima na kuganizila zimene zam’pangitsa kuti akambe kapena kucita zimenezo. Ganizilaninso zotulukapo za zimene mufuna kucita.—Miy. 19:11

  • Kumbukilani kuti tonse ndise opanda ungwilo, ndipo nthawi zina tingakambe kapena kucita zinthu zimene pambuyo pake tingadziimbe nazo mlandu

  • Mukasemphana maganizo, muzithetsa nkhani mwamsanga

TAMBANI VIDIYO YAKUTI MUZIKONDANA”PEWANI KUNYADA NDI KUCITA ZOSAYENELA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi m’bale Larry anaonetsa bwanji kuti sanakondwele na lingalilo la m’bale Tom?

  • Kodi kuyamba waima kuti aganizilepo kunam’thandiza bwanji mbale Tom kuti apewe kukwiya?

  • Kodi kuyankha modekha kwa m’bale Tom kunathandiza bwanji?

Kodi mpingo umapindula bwanji ngati tikhalabe odekha wina akatikwiyitsa?