Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kuteteza Mgwilizano Wathu Wapadela

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Usiku wakuti maŵa Yesu aphedwa, anapemphela kuti ophunzila ake “akhale mu umodzi weni-weni.” (Yoh. 17:23) Kuti tikhale ogwilizana, tifunika kuonetsana cikondi cimene “sicisunga zifukwa.”—1 Akor. 13:5.

MMENE TINGACITILE:

  • Tengelani citsanzo ca Yehova mwa kuyang’ana zabwino mwa ena

  • Muzikhululukila ena na mtima wonse

  • Mukakambilana ndipo nkhaniyo yatha, osaiutsanso.—Miy. 17:9

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI MUZIKONDANA”—MUSAMASUNGE ZIFUKWA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • M’mbali yoyamba ya vidiyo, kodi Helen anaonetsa bwanji kuti anali ‘kusunga zifukwa’?

  • M’mbali yaciŵili ya vidiyo, kodi Helen anacita ciani kuti agonjetse maganizo oipa na kukhala na maganizo oyenela?

  • Kodi Helen anathandizila bwanji kuti mpingo ukhale wogwilizana?

N’ndani amene amavulazika kwambili ngati tisunga zifukwa?